5 ndipo m'mene anawerama cosuzumira anaona nsaru zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo.
6 Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsaru zabafuta zitakhala,
7 ndi mlezo, umene unali pamutu pace, wosakhala pamodzi ndi nsaru zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.
8 Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupira.
9 Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera iye kuuka kwa akufa.
10 Cifukwa cace akuphunzirawo anacokanso, kunka kwao.
11 Koma Mariya analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama cisuzumirire kumanda;