10 Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano,
11 Cifukwa cace Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda Iodzala ndi nsomba zazikuru, zana limodzi, ndi makumiasanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinacuruka kotere, kokha silinang'ambika.
12 Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa akuphunzira anatha kumfunsa iye, Ndinu yani? podziwa kuti ndiye Ambuye.
13 Yesu anadza natenga mkate napatsa Iwo, momwemonso nsomba.
14 Imeneyo ndi nthawi yacitatu yakudzionetsera Yesu kwa akuphunzira ace, m'mene atauka kwa akufa.
15 Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa ana a nkhosa anga.
16 Ananena nayenso kaciwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.