10 Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi?
11 Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula cimene ticidziwa, ndipo ticita umboni za cimene taeiona; ndipo umboni wathu simuulandira.
12 Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?
13 Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma iye wotsikayo kucokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m'Mwambayo.
14 Ndipo monga Mose anakweza njoka m'cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa;
15 kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa iye.
16 Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.