24 Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende.
25 Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ace a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe.
26 Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Y ordano, amene munamcitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa iye.
27 Yohane anayankha nati, Munthu sakhoza kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kocokera Kumwamba.
28 Inu nokha mundicitira umboni, kuti ndinati, Sindine Kristu, koma kuti ndiri wotumidwa m'tsogolo mwace mwa iye.
29 Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzace wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukuru cifukwa ca mau a mkwatiyo; cifukwa cace cimwemwe canga cimene cakwanira.
30 Iyeyo ayenera kukula koma ine ndicepe.