30 Iyeyo ayenera kukula koma ine ndicepe.
31 Iye wocokera Kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wocokera Kumwamba ali woposa onse.
32 Cimene anaciona nacimva, acita umboni wa ici comwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wace.
33 1 Iye amene analandira umboni wace anaikapo cizindikilo cace kuti Mulungu ali woona.
34 Pakuti 2 Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti 3 sapatsa Mzimu ndi muyeso.
35 4 Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lace.
36 Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.