3 M'menemo munagona khamu lalikuru la anthu odwala akhungu, opunduka miyendo, opuwala. [
4 ]
5 Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwace zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.
6 Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikuru pamenepo, ananena naye, Ufuna kuciritsidwa kodi?
7 Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndiribe wondibvika ine m'thamanda, pali ponse madzi abvundulidwa; koma m'mene ndirinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.
8 Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende,
9 Ndipo pomwepo munthuyu anacira, nayalula mphasa yace, nayenda.Koma tsiku lomwelo linali la Sabata.