1 Zitapita izi anacoka Yesu kunka ku tsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiya,
2 Ndipo khamu lalikuru la anthu linamtsata iye, cifukwa anaona zizindikilo zimene anacita pa odwala.
3 Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.
4 Ndipo Paskha, phwando la Ayuda, anayandikira.
5 Pamenepo Yesu, pokweza maso ace, ndi kuona kuti khamu lalikuru lirinkudza kwa iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?
6 Koma ananena ici kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha cimene adzacita.
7 Filipo anayankha iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.