31 Atate athu anadya mana m'cipululu; monga kwalembedwa, Mkate wocokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya,
32 Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.
33 Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kucokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.
34 Pamenepo anati kwa iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.
35 Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
36 Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.
37 Cinthu conse cimene anandipatsa Ine Atate cidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.