13 Cinkana anatero panalibe munthu analankhula za iye poyera, cifukwa ca kuopa Ayuda.
14 Koma pamene padafika pakati pa phwando, Yesu anakwera nalowa m'Kacisi, naphunzitsa,
15 Cifukwa cace Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?
16 Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, koma ca iye amene anandituma Ine.
17 Ngati munthu ali yense afuna kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco, ngati cicokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zocokera kwa Ine ndekha.
18 Iye wolankhula zocokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha, iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa iye mulibecosalungama.
19 Si Mose kodi anakupatsani inu cilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu acita cilamulo? Mufuna kundipha cifukwa ninji?