23 Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti cilamulo ca Mose cingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, cifukwa ndamciritsadi munthu tsiku la Sabata?
24 Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani ciweruziro colungama.
25 Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha r
26 ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akuru adziwa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?
27 Koma ameneyo tidziwa uko acokera: koma Kristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko acokera.
28 Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.
29 Ine ndimdziwa iye; cifukwa ndiri wocokera kwa iye, nandituma Ine Iyeyu.