29 Ine ndimdziwa iye; cifukwa ndiri wocokera kwa iye, nandituma Ine Iyeyu.
30 Pamenepo anafuna kumgwira iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, cifukwa nthawi yace siinafike.
31 Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira iye; ndipo ananena, Pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita ameneyo?
32 Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire iye.
33 Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma Ine.
34 Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo.
35 Cifukwa cace Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza iye? kodi adzamuka kwa Ahelene obalalikawo, ndi kuphunzitsa Ahelene?