22 Cifukwa cace Ayuda ananena, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?
23 Ndipo ananena nao, Inu ndinu ocokera pansi; Ine ndine wocokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindiri Ine wa dziko lino lapansi.
24 Cifukwa cace ndinati kwa inu, kuti mudzafam'macimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'macimo anu.
25 Pamenepo ananena kwa iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Cimene comwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira paciyambi.
26 Ndiri nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa iye, zomwezo ndilankhuia kwa dziko lapansi.
27 Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate.
28 Cifukwa cace Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindicita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.