30 Pakulankhula iye zimenezi, ambiri anakhulupirira iye.
31 Cifukwa cace Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli akuphunzira anga ndithu;
32 ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.
33 Anamyankha iye, Tiri mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yonse; munena bwanji; Mudzayesedwa aufulu?
34 Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo.
35 Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.
36 Cifukwa cace ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.