13 Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israyeli. Cifukwa cace tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.
14 Koma iye sadafuna kumvera mau ace, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkangamiza, nagona naye.
15 Atatero Amnoni anadana naye ndi cidani cacikuru kopambana; pakuti cidani cimene anamuda naco, cinali cacikuru koposa cikondi adamkonda naco. Ndipo Amnoni ananena naye, Nyamuka, coka.
16 Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti coipa ici cakuti ulikundipitikitsa ncacikuru coposa cina cija unandicitira ine. Kama anakana kumvera.
17 Pomwepo anaitana mnyamata wace amene anamtumikira, nati, Turutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze citseko atapita iye.
18 Ndipo iye anabvala cobvala ca mawanga mawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amabvala zotere. Ndipo mnyamata wace anamturutsa, napiringidza citseko atapita iye.
19 Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pace, nang'amba cobvala ca mawanga mawanga cimene analikubvala, nagwira dzanja lace pamutu pace, namuka nayenda, nalira komveka.