8 Pakuti nkhondo inatanda pa dziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga.
9 Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yace, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkuru. Ndipo mutu wace unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye Inapitirira.
10 Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yoabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.
11 Ndipo Yoabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? ndipo ine ndikadakupatsa ndarama khumi ndi lamba.
12 Munthuyo nanena ndi Yoabu, Ndingakhale ndikalandira ndarama cikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi ltai, kuti, Cenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.
13 Ndikadacita conyenga pa moyo wace, palibe mrandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsuta.
14 Pomwepo Yoabu anati, Sindiyenera kucedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.