30 Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere ku nyumba yace.
31 Ndipo Barizilai, Mgileadi anatsika kucokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordano ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordano.
32 Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.
33 Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.
34 Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kumka ku Yerusalemu?
35 Lero ndiri nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira cimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oyimba? Cifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.
36 Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordano pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphothoyotere?