2 Samueli 19:5-11 BL92

5 Ndipo Yoabu anafika ku nyumba ya mfumu, nati, Lero mwacititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu amuna ndi akazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu ang'ono;

6 m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu.

7 Cifukwa cace tsono nyamukani, muturuke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kuturuka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo cimeneci cidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.

8 Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pacipata, Ndipo inauza anthu kuti, Onani mfumu irikukhala pacipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisrayeli adathawa, munthu yense ku hema wace.

9 Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israyeli analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.

10 Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Cifukwa cace tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?

11 Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akuru a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu ku nyumba yace? pakuti mau a Aisrayeli onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo ku nyumba yace.