11 Ndipo anauza Davide cimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Sauli anacita.
12 Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace kwa anthu a ku Jabezi Gileadi amene anawaba m'khwalala la Betisani, kumene Afilisti adawapacika, tsiku lija Afilistiwo anapha Sauli ku Giliboa;
13 nacotsa kumeneko mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapacikidwa.
14 Naika mafupa a Sauli ndi Jonatani mwana wace ku dziko la Benjamini m'Zela, m'manda a Kisi atate wace; nacita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pace Mulungu anapembedzeka za dzikolo.
15 Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisrayeli; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ace pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.
16 Ndipo Isibenobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wace kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anabvala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
17 Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfliistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzaturuka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israyeli.