12 Koma iyeyoanaima pakati pa mundawo, naucinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru.
13 Ndipo atatu a mwamakumi atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti Gnamanga zithando m'cigwa ca Refaimu.
14 Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali m'Betelehemu.
15 Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! wina akadandipatsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri pacipatapo!
16 Ndipongwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, nizitunga madzi m'citsime ca ku Betelehemu, ca pa cipataco, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafuna kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.
17 Nati, Ndisacite ici ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa ana pitawa ndi kutaya moyo wao? Cifukwa cace iye anakana kumwa. Izi anazicita ngwazi zitatuzi.
18 Ndipo Abisai, mbale wa Yoabu, mwana wa Zeruya, anali wamkuru wa atatuwa. Iye natukula mkondo wace pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.