17 Nati, Ndisacite ici ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa ana pitawa ndi kutaya moyo wao? Cifukwa cace iye anakana kumwa. Izi anazicita ngwazi zitatuzi.
18 Ndipo Abisai, mbale wa Yoabu, mwana wa Zeruya, anali wamkuru wa atatuwa. Iye natukula mkondo wace pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.
19 Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? cifukwa cace anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikana ndi atatu oyamba.
20 Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabzeli amene anacita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Moabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya cipale cofewa;
21 ndipo anapha M-aigupto munthu wokongola, M-aigupto anali nao mkondo m'dzanja lace; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wa iye mwini.
22 Izi anacita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.
23 Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikana ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ace.