1 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israyeli, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israyeli ndi Yuda.
2 Ndipo mfumu inanena ndi Yoabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israyeli, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kucuruka kwao kwa anthu.
3 Ndipo Yoabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwacurukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu acione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi cinthu ici?
4 Koma mau a mfumu anapambana Yoabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yoabu ndi atsogoleri a khamulo anaturuka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israyeli.
5 Naoloka Yordano, namanga zithando ku Aroeri ku dzanja lamanja kwa mudzi uli pakati pa cigwa ca Gadi, ndi ku Jazeri;
6 nafika ku Gileadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Jaana ndi kuzungulira, kufikira ku Zidoni,
7 nafika ku linga la Turo ndi ku midzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; naturukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.