12 Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obedi-Edomu ndi zace zonse, cifukwa ca likasa la Mulungu. Comweco Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu, nakwera nalo ku mudzi wa Davide, ali ndi cimwemwe.
13 Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi conenepa cina.
14 Ndipo Davide anabvina ndi mphamvu yace yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.
15 Comweco Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anakwera nalo likasa la Yehova, ndi cimwemwe ndi kulira kwa malipenga,
16 Ndipo kunali pamene likasa la Yehova tinafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikubvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwace.
17 Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analgka pamalo pace pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.
18 Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu.