1 Ndipo m'tsogolo mwace Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa; Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
2 Ndipo anakantha Amoabu nawayesa ndi cingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi cingwe cimodzi cathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera: nayo mitulo.
3 Davide anakanthanso Hadadezeri, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wace ku cimtsinje ca Firate.
4 Ndipo Davide anatenga apakavalo ace cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi maku mi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magareta, koma anasunga a iwo akufikira magareta zana limodzi.