12 Ndipo tsopano, Israyeli, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanundimtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,
13 kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?
14 Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse ziri m'mwemo ndi zace za Yehova Mulungu wanu.
15 Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.
16 Potero dulani khungu la mitima yanu, ndipo musamapulukiranso.
17 Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye ya ambuye; Mulungu wamkuru, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira cokometsera mlandu.
18 Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa cakudya ndi cobvala.