1 Ndipo Mose anamuka nanena mau awa kwa Israyeli wonse,
2 nati nao, Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lero lino; sindikhozanso kuturuka ndi kulowa ndipo Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordano uyu.
3 Yehova Mulungu wanu ndiye adzaoloka pamaso panu, iye ndiye adzaononga amitundu awo pamaso panu, ndipo mudzawalandira. Yoswa ndiye adzakutsogolerani pooloka, monga ananena Yehova.
4 Ndipo Yehova adzawacitira monga anacitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga.
5 Yehova akadzawapereka pamaso panu, muziwacitira monga mwa lamulo lonse ndakuuzani.
6 Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamacita mantha, kapena kuopsedwa cifukwa ca iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusowani, kapena irukusiyani.
7 Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israyeli wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.
8 Ndipo Yehova, iye ndiye amene akutsogolera; iye adzakhala ndi iwe, iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamacita mantha, usamatenga nkhawa.
9 Ndipo Mose analembera cilamulo ici, nacipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kwa akuru onse a Israyeli,
10 Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m'caka cakulekerera, pa madyerero a misasa;
11 pakufika Israyeli wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira cilamulo ici pamaso pa Israyeli wonse, m'makutu mwao.
12 Sonkhanitsan; anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kucita mau onse a cilamulo ici;
13 ndi kuti ana ao osadziwa amve, oaphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordano kulilandira likhale lanu lanu.
14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'cihema cokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'cihema cokomanako.
15 Ndipo Yehova anaoneka m'cihema, m'mtambo njo; ndipo mtambo njo unaima pa khomo la cihema.
16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, oadzatsata ndi cigololo milungu yacilendo ya dziko limene analowa pakati pace, nadzanditava Ine, ndi kutyola cipangano canga ndinapangana naoco.
17 Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zobvuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?
18 Koma Ine ndidzabisatu nkhope yanga tsiku lija cifukwa ca zoipa zonse adazicita; popeza anadzitembenukira milungu yina.
19 Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israyeli iyi: mulike m'kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indicitire mboni yotsutsa ana a Israyeli.
20 Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu yina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kutyola cipangano canga.
21 Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zobvuta zambiri, nyimbo iyi idzacita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azicita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.
22 Potero Mose analembera nyimboyi tsiku lomweli, naiphunzitsa ana a Israyeli.
23 Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israyeli m'dziko limene ndinawalumbirira: ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.
24 Ndipo kunali, Mose atatha kulembera mau a cilamulo ici m'buku, kufikira atalembera onse,
25 Mose anauza Alevi akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kuti,
26 Landirani buku ili la cilamulo, nimuliike pambali pa likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.
27 Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova: koposa kotani nanga nditamwalira ine!
28 Ndisonkhanitsire akuru onse a mapfuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kucititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.
29 Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo cidzakugwerani coipa masiku otsiriza; popeza mudzacita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace ndi nchito za manja anu.
30 Ndipo Mose ananena mau a nyimbo iyi m'makutu mwa msonkhano wonse wa Israyeli, kufikira adatha.