Deuteronomo 4 BL92

Mose awadandaulira amvere Malamulo a Mulungu

1 Ndipo tsopano, Israyeli, dioloketu tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwacite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.

2 Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kucotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani.

3 Maso anu anapenya cocita Yehova cifuwa ca Baala Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala Peori, Yehova Mulungu wanu anawaononga pakati panu.

4 Koma inu amene munamamatira Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo nonsenu lero lomwe.

5 Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzicita cotero pakati pa dziko limene mumkako kulilandira likhale lanu Lanu.

6 Cifukwa cace asungeni, aciteni; pakuti ici ndi nzeru zanu ndi cidziwitso canu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukuru uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira.

7 Pakuti dioloketu mtundu waukuru wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pao monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene pali ponse timaitanira iye?

8 Ndipo mtundu waukuru wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga cilamulo ici conse ndiciika pamaso panu lero lino?

9 Cokhaci, dzicenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwacangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisacoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.

10 Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'Horebe muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo pa dziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.

11 Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde pa phiri; ndi phizilo linayaka mota kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.

12 Pamenepo Yehova ananena ndi inu ali pakati pa moto; munamva kunena kwa mau, osaona maonekedwe, koma kunenako.

13 Pamenepo anakufotokozerani cipangano cace, cimene anakulamulirani kucicita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.

14 Ndipo Yehova anandilamulira muja ndikuphunzitseni malemba ndi maweruzo, kuti mukawacite m'dziko limene muolokerako kulilandira likhale lanu lanu.

15 Potero dzicenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenya mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu m'Horebe, ali pakati pa moto;

16 kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga cifaniziro ciri conse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi;

17 mafanidwe a nyama iri yonse iri pa dziko lapansi, mafanidwe a mbalame iri yonse yamapiko yakuuluka m'mlengalenga,

18 mafanidwe a cinthu ciri conse cokwawa pansi, mafanidwe a nsomba iri yonse yokhala m'madzi pansi pa dziko;

19 ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.

20 Koma Yehova anakutengani, nakuturutsani m'ng'anjo yamoto, m'Aigupto, mukhale kwa iye anthu a colowa cace, monga mukhala lero lino.

21 Yehova anakwiyanso nane cifukwa ca mau anu, nalumbira kuti sindidzaoloka Yordano ine, ndi kuti sindidzalowa m'dziko lokomali Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu;

22 pakuti ndidzafa m'dziko muno, osaoloka Yordano; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanu lanu.

23 Dzicenjerani, mungaiwale cipangano ca Yehova Mulungu wanu, cimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, cifaniziro ca kanthu kali konse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.

24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.

25 Mutakabala ana, ndi zidzukulu, ndipo mutakakhala nthawi yaikuru m'dzikomo, ndi kudziipsa, ndi kupanga fano losema, m'cifaniziro ca kanthu kali konse, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace:

26 ndiitana kumwamba ndi dziko lapansi zicite mboni pa inu lero lino, kuti mudzaonongeka msangatu kucotsedwa ku dziko limene muolokera Yordano kulilandira likhale lanu lanu; masiku anu sadzacuruka pamenepo, koma mudzaonongeka konse.

27 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.

28 Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, nchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.

29 Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

30 Mukakhala nao msauko, zikakugwerani zonsezi, masiku otsiriza mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvera mau ace;

31 popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wacifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala cipangano ca makolo anu cimene analumbirira iwo.

32 Pakuti, funsiranitu, masiku adapitawo, musanakhale inu, kuyambira tsikuli Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi, ndi kuyambira malekezero ena a thambo kufikira malekezero anzace a thambo, ngati cinthu cacikuru conga ici cinamveka, kapena kucitika?

33 Kodi pali mtundu wa anthu udamva a Malungu akunena pakati pa moto, monga mudamva inu, ndi kukhala ndi moyo?

34 Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikilo, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikuru, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakucitirani m'Aigupto pamaso panu?

35 Inu munaciona ici, kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu; palibe wina wopanda iye.

36 Anakumvetsani mau ace kucokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo pa dziko lapansi anakuonetsani moto wace waukuru; nimunamva mau ace pakati pa moto.

37 Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakuturutsani pamaso pace ndi mphamvu yace yaikuru, m'Aigupto;

38 kupitikitsa amitundu akuru ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale colowa canu, monga lero lino.

39 Potero dziwani lero tino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi pa dziko lapansi; palibe wina.

40 Muzisunga malemba ace, ndi malamulo ace, amene ndikuzuzani lero lino, kuti cikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu acuruke pa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.

Midzi itatu yopulumukirako kum'mawa kwa Yordano

41 Pamenepo Mose anapatula midzi itatu tsidya lija la Yordano loturuka dzuwa;

42 kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wace dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo:

43 ndiyo Bezere, m'cipululu, m'dziko lacidikha, ndiwo wa Anrubeni; ndi Ramoti m'Gileadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basana, ndiwo wa Amanase.

44 Ndipo ici ndi cilamulo Mose anaciika pamaso pa ana a Israyeli;

45 izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israyeli, poturuka iwo m'Aigupto;

46 tsidya lija la Yordano, m'cigwa ca pandunji pa Beti Peori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israyeli anamkantha, poturuka iwo m'Aigupto;

47 ndipo analanda dziko lace, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordano loturuka dzuwa;

48 kuyambira ku Aroeri, ndiwo m'mphepete mwa mtsinje wa Arinoni, kufikira phiri la Sioni (ndilo Herimoni),

49 ndi cidikha conse tsidya lija la Yordana kum'mawa, kufikira nyanja ya kucidikha, pa tsinde lace la Pisiga.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34