Deuteronomo 15 BL92

Za caka ca cilekerero

1 Pakutha Pace pa zaka zisanu ndi ziwiri pakhale cilekerero.

2 Cilekereroco ndici: okongoletsa onse alekerere cokongoletsa mnansi wace; asacifunse kwa mnansi wace, kapena mbale wace; popeza analalikira cilekerero ca Yehova.

3 Muyenera kucifunsa kwa mlendo; koma canu ciri conse ciri ndi mbale wanu, dzanja lanu licilekerere;

4 ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu;

5 cokhaci mumvere cimverere mau a Yehova Mulungu wanu, kuti musamalire kucita malamulo awa onse amene ndikuuzani lero lino.

6 Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monza ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzacita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzacita ufumu pa inu.

Za aumphawi ndi aka polo

7 Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wilia wa abale anu, m'umodzi wa midzi yanu, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi;

8 koma muzimtansira dzanjalanundithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwace, monga umo amasowa.

9 Dzicenjerani, mungakhale mau opanda pace mumtima mwanu, ndi kuti, Cayandika caka cacisanu ndi ciwiri, caka ca cilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale cimo.

10 Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, cifukwa ca ici Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu nchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.

11 Popeza waumphawi salekana m'dziko, cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.

12 Mukagula mbale wanu, Mhebri wamwamuna kapena Mhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi cimodzi; koma caka cacisanu ndi ciwiri umlole acoke kwanu waufulu.

13 Ndipo pomlola iwe acoke kwanu waufulu, musamamlola acoke wopanda kanthu;

14 mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za padwale, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.

15 Ndipo mukumbukile kuti munali akapolo m'dziko la Aigupto, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; cifukwa cace ndikuuzani ici lero lino.

16 Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituruka kucoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;

17 pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwace, kulikanikiza ndi citseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzicitanso momwemo ndi adzakazi anu.

18 Musamayesa neosautsa, pomlola akucokereni waufulu; popeza anakugwirirani nchito zaka zisanu ndi cimodzi monga wolipidwa wakulandira cowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzicita.

Za nyama zoyamba kubadwa

19 Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa nchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.

20 Muzidye caka ndi caka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene Yehova adzasankha, inu ndi a m'banja mwanu.

21 Koma ikakhala naco cirema, yotsimphina, kapena yakhungu, cirema ciri conse coipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.

22 Muidye m'mudzi mwanu; odetsa ndi oyera aidye cimodzimodzi, monga mphoyo ndi nswala.

23 Mwazi wace wokha musamadya; muuthire pansi ngati madzi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34