Deuteronomo 32 BL92

Nyimbo adailemba Mose

1 Kumwamba kuchere khutu, ndipo ndidzanena;Ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga;

2 Ciphunzitso canga cikhale ngati mvula;Maneno anga agwe ngati mame;Ngati mvula yowaza pamsipu,Ndi monga madontho a mvula pazitsamba.

3 Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova;Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.

4 Thanthwe, nchito yace ndi yangwiro;Pakuti njira zace zonse ndi ciweruzo;Mulungu wokhulupirika ndi wopanda cisalungamo;Iye ndiye wolungama ndi wolunjika,

5 Anamcitira zobvunda si ndiwo ana ace, cirema ncao;Iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.

6 Kodi mubwezera Yehova cotero,Anthu inu opusa ndi opanda nzeru?Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuyewanu;Anakulengani, nakukhazikitsani?

7 Kumbukirani masiku akale,Zindikirani zaka za mibadwo yambiri;Funsani atate wanu, adzakufotokozerani;Akuru anu, adzakuuzani.

8 Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu colowacao,Pamene anagawa ana a anthu,Anaika malire a mitundu ya anthu,Monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israyeli,

9 Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ace;Yakobo ndiye muyeso wa colowacace.

10 Anampeza m'dziko la mabwinja, ndi m'cipululu colira copanda kanthu;Anamzinga, anamlangiza,Anamsunga ngati kamwana lea m'diso;

11 Monga mphungu ikasula cisa cace,Nikapakapa pa ana ace,Iye anayala mapiko ace, nawalandira,Nawanyamula pa mapiko ace;

12 Yehova yekha anamtsogolera,Ndipo palibe mulungu wacilendo naye.

13 Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi,Ndipo anadya zipatso za m'minda;Namyamwitsa uci wa m'thanthwe,Ndi mafutam'mwala wansangalabwe;

14 Mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa,Ndi mafuta a ana a nkhosa,Ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basana, ndi atonde,Ndi imso zonenepa zatirigu;Ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa,

15 Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira;Wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta;Pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga,Napeputsa thanthwe la cipulumutso cace.

16 Anamcititsa nsanje ndi milungu yacilendo,Anautsa mkwiyo wace ndi zonyansa.

17 Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai;Milungu yosadziwa iwo,Yatsopano yofuma pafupi, Imene makolo anu sanaiopa,

18 Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,Mwaiwala Mulungu amene anakulengani.

19 Ndipo Yehova anaciona, nawanyoza,Pakuipidwa nao ana ace amuna, ndi akazi.

20 Ndipo iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga,Ndidzaona kutsiriza kwao;Popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira,Ana osakhulupirika iwo.

21 Anautsa nsanje yanga ndi cinthu cosati Mulungu;Anautsa mkwiyo wanga om zopanda pace zao.Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu;Ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.

22 Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga,Utentha kumanda kunsiUkutha dziko lapansi ndi zipatso zaceNuyatsa maziko a mapiri,

23 Ndidzawaunjikira zoipa;Ndidzawathera nubvi yanga.

24 Adzaonda nayo njalaAdzanyekeka ndi makala a moto, cionongeko cowawa;Ndipo ndidzawatumizira mana a zirombo,Ndi ululu wa zokwawa m'pfumbi.

25 Pabwalo lupanga lidzalanda,Ndi m'zipinda mantha;Lidzaononga mnyamata ndi namwali,Woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.

26 Ndinati, Ndikadawauzira ndithu,Ndikadafafaniza cikumbukiro cao mwa anthu;

27 Ndikadapanda kuopa mkwiyo wapamdani,Angayese molakwa outsana nao,Anganene, Lakwezeka dzanja lathu,Ndipo Yehova sanacita ici conse.

28 Popeza iwo ndiwo mtundu wa anthu wosowa uphungu konse,Ndipo alibe cidziwitso.

29 Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ici,Akadasamalira citsirizo cao!

30 Mmodzi akadapitikitsa zikwi,Awiri akadathawitsa zikwi khumi,Akadapanda kuwagulitsa Thanthwelao,Akadapanda kuwapereka Yehova.

31 Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu,Oweruza a pamenepo ndiwo adani athu.

32 Pakuti mpesa wao ndiwo wa ku Sodomu,Ndi wa m'minda ya ku Gomora;Mphesa zao ndizo mphesa zandulu,Matsangwi ao ngowawa.

33 Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka,Ndi ululu waukali wa mphiri.

34 Kodi sicisungika ndi Ine,Colembedwa cizindikilo mwa cuma canga ceni ceni?

35 Kubwezera cilango nkwanga, kubwezera komwe,Pa nyengo ya kuterereka phazi lao;Pakuti tsiku la tsoka lao layandika,Ndi zinthu zowakonzeratu zifulomira kudza.

36 Popeza Yehova adzaweruza anthuace,Nadzacitira nsoni anthu ace;Pakuona iye kuti mphamvu yao yatha,Wosatsala womangika kapena waufulu,

37 Pamenepo adzati, Iri kuti milunguyao,Thanthwe limene anathawirako?

38 Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera,Nimwa vinyo wa nsembe yao yothira?Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu.

39 Tapenyani tsopano kuti Ine ndine iye,Ndipo palibe mulungu koma Ine;Ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi mayo:Ndikantha, ndicizanso Ine;Ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.

40 Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba,Ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha,

41 Ndikanola lupanga langa lonyezimira,Ndi dzanja langa likagwira ciweruzo;Ndidzabwezera cilango ondiukira,Ndi kulanga ondida.

42 Mibvi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi,Ndi lupanga langa lidzalusira nyama;Ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa,Ndi mutu wacitsitsi wa mdani,

43 Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ace;Adzalipsira mwazi wa atumiki ace,Adzabwezera cilango akumuukira,Nadzafafanizira zoipa dziko lace, ndi anthu ace.

44 Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Hoseya mwana wa Nuni.

45 Ndipo Mose anatha kunena mau awa onse kwa Israyeli wonse;

46 nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikucitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwacita mau onse a cilamulo ici.

47 Pakuti sicikhala kwa inu cinthu copanda pace, popeza ndico moyo wanu, ndipo mwa cinthu ici mudzacurukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordano, kulilandira.

Mulungu auza Mose akwere m'phiri la Nebo

48 Ndipo Yehova ananena ndi Mose tsiku lomweli, ndi kuti,

49 Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Moabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israyeli likhale lao lao;

50 nufe m'phiri m'mene ukweramo, nuitanidwe kumka kwa anthu a mtundu wako; monga Aroni mbale wako anafa m'phiri la Hori, naitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace;

51 popeza munandilakwira pakati pa ana a Israyeli ku madzi a Meriba wa Kadesi m'cipululu ca Zini, popeza simunandipatula Ine pakati pa ana a Israyeli,

52 Pakuti udzapenya dzikoli pandunji pako; koma osalowako ku dziko limene ndipatsa ana a Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34