Deuteronomo 21 BL92

Za wophedwa mosadziwika

1 Akapeza munthu waphedwa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu, nagona pamunda, wosadziwika wakumkantha,

2 pamenepo azituruka akuru anu ndi oweruza anu, nayese ku midzi yomzinga wophedwayo;

3 ndipo kudzali kuti mudzi wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akuru a mudzi uwu atenge ng'ombe yamsoti yosagwira nchito, yosakoka goli;

4 ndipo akuru a mudzi uwu atsike nao msotiwo ku cigwa coyendako madzi, cosalima ndi cosabzala, naudula khosi msotiwo m'cigwamo;

5 ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m'dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.

6 Ndipo akuru onse a mudziwo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa msoti woudula khosi m'cigwamo;

7 nayankhe nati, Manja athu sanakhetsa mwazi uwu, ndi maso athu sanauona.

8 Landirani, Yehova, cotetezera anthu anu Israyeli, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosacimwa ukhale pakati pa anthu anu Israyeli; ndipo adzawatetezera ca mwaziwo.

9 Cotero mudzicotsere mwazi wosacimwa pakati panu, pakuti wacita coyenera pamaso pa Yehova.

Za akazi otengedwa kunkhondo

10 Pamene muturuka kumka ku nkhondo ya pa adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu awapereka m'manja mwanu, ndipo muwagwira akhale akapolo anu;

11 mukaona mwa akapolowa mkazi wokongola, mukamkhumba, ndi kufuna kumtenga akhale mkazi wanu;

12 pamenepo mufike naye kwanu ku nyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pace, ndi kuwenga makadabo ace;

13 nabvule zobvala za ukapolo wace, nakhale m'nyumba mwanu, nalire atate wace, ndi mai wace mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wace, ndi iye akhale mkazi wanu.

14 Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa cuma, popeza wamcepetsa.

Mphamvu ya oyamba kubadwa

15 Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;

16 pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ace amuna cuma cace, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.

17 Koma azibvomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lace la zace zonse; popeza iye ndiye ciyambi ca mphamvu yace; zoyenera woyamba kubadwa nzace.

Za ana opulukira osamvera

18 Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wace, kapena mau a mai wace, wosawamvera angakhale anamlanga;

19 azimgwira atate wace ndi mai wace, ndi kuturukira naye kwa akuru a mudzi wace, ndi ku cipata ca malo ace;

20 ndipo anene kwa akulu a mudzi wace, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.

21 Pamenepo amuna onse a mudzi wace amponye miyala kuti afe; cotero mucotse coipaco pakati panu; ndipo Israyeli wonse adzamva, nadzaopa.

Za kuika wophedwa mompacika

22 Munthu akakhala nalo cimo loyenera imfa, kuti amuphe, ndipo wampacika;

23 mtembo wace usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopacikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34