1 Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zirikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.
2 Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu ku nyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo.
3 Mutero nayenso buru wace; mutero naconso cobvala cace; mutero naconso cotayika ciri conse ca mbale wanu, cakumtayikira mukacipeza ndi inu; musamazilekerera.
4 Mukapenya buru kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.
5 Mkazi asabvale cobvala ca mwa muna, kapena mwamuna asabvale cobvala ca mkazi; pakuti ali yense wakucita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.
6 Mukacipeza cisa ca mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi mace alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga mace pamodzi ndi ana;
7 muloletu mace amuke, koma mudzitengere ana; kuti cikukomereni, ndi kuti masiku anu acuruke.
8 Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lace, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.
9 Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe.
10 Musamalima ndi buru ndi ng'ombe zikoke pamodzi.
11 Musamabvala nsaru yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje.
12 Mudzipangire mphonje pa ngondya zinai za copfunda canu cimene mudzipfunda naco.
13 Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda,
14 namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana nave sindinapeza zizindikilo zakuti ndiye namwali ndithu;
15 pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wace azitenga ndi kuturuka nazo zizindikilo za unamwali wace wa namwaliyo, kumka nazo kwa akuru a mudzi kucipata;
16 ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akuru, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace, koma amuda;
17 ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikilo za unamwali wace in'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikilo za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula cobvalaco pamaso pa akulu a mudziwo.
18 Pamenepo akuru a mudziwo azitenga munthuyu ndi kumkwapula;
19 ndi kumlipitsa masekeli makumi okha okha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israyeli, ndipo azikhala mkazi wace, sakhoza kumcotsa masiku ace onse.
20 Koma cikakhala coona ici, kuti zizindikilo zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo;
21 pamenepo azimturutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wace, ndipo amuna a mudzi wace azimponya miyala kuti afe; popeza anacita copusa m'Israyeli, kucita cigololo m'nyumba ya atate wace; cotero uzicotsa coipaco pakati panu.
22 Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; cotero muzicotsa coipaco mwa Israyeli.
23 Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mudzi mwamuna, nagona nave;
24 muziwaturutsa onse awiri kumka nao ku cipata ca mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanapfuula angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anacepetsa mkazi wa mnansi wace; cotero muzicotsa coipaco pakati panu.
25 Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye;
26 koma namwaliyo musamamcitira kanthu; namwaliyo alibe cimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzace namupha;
27 pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anapfuula, koma panalibe wompulumutsa.
28 Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, oakamgwira nagona naye, napezedwa iwo,
29 pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wace wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wace; popeza anamcepetsa; sakhoza kumcotsa masiku ace onse.
30 Munthu asatenge mkazi wa atate wace, kapena kubvula atate wace.