Deuteronomo 20 BL92

Malamulo a kunkhondo

1 Pamene muturuka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magareta ndi anthu akucurukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ali ndi inu.

2 Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu,

3 nati nao, Tamverani, Israyeli, muyandikiza kunkhondo lero paadani anu; musalumuka mitima yanu; musacita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;

4 pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.

5 Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.

6 Ndipo ndani munthuyo ananka munda wamphesa osalawa zipatso zace? amuke nabwerere ku nyumba yace, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zace.

7 Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? amuke nabwerere kunyumba kwace, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.

8 Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakucita mantha ndi wofumuka mtima? amuke nabwerere kunyumba kwace, ingasungunuke mitima ya abale ace monga mtima wace.

9 Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu.

10 Pamene muyandikiza mudzi kucita nao nkhondo, muziupfuulira ndi mtendere.

11 Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opereka m'mwemo akhale alambi anu, nadzakutumikirani.

12 Koma ukapanda kucita zamtendere ndi inu, koma kucita nkhondo nanu, pamenepo uumangire tsasa.

13 Ndipo pamene Yehova Mulungu wanu aupereka m'dzanja lanu, mukanthe amuna ace onse ndi lupanga lakuthwa.

14 Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse ziti m'mudzimo, zankhondo zace zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

15 Muzitero nayo midzi yonse yokhala kutaritari ndi inu, yosakhala midzi ya amitundu awa.

16 Koma za midzi ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale colowa canu, musasiyepo camoyo ciri conse cakupuma;

17 koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;

18 kuti angakuphunzitseni kucita monga mwa zonyansa zao zonse, amazicitira milungu yao; ndipo mungacimwire Yehova Mulungu wanu.

19 Pamene mumangira tsasa mudzi masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yace ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m'munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa?

20 Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mudzi wocita nanu nkhondo muumangire macemba, mpaka mukaugonjetsa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34