1 Ndipo mdalitso, Mose munthu wa Mulungu anadalitsa nao ana a Israyeli asanafe, ndi uwu.
2 Ndipo anati,Yehova anafuma ku Sinai,Nawaturukiraku Seiri;Anaoneka wowala pa phiri la Parana,Anafumira kwa opatulika zikwi zikwi;Ku dzanja lamanja lace kudawakhalira lamulo lamoto.
3 Inde akonda mitundu ya anthu;Opatulidwa ace onse ali m'dzanjamwanu;Ndipo akhala pansi ku mapazi anu;Yense adzalandirako mau anu.
4 Mose anatiuza cilamulo,Colowa ca msonkhano wa Yakobo.
5 Ndipo iye anali mfumu m'Yesuruni,Pakusonkhana mafumu a anthu,Pamodzi ndi mapfuko a Israyeli.
6 Rubeni akhale ndi moyo, asafe,Koma amuna ace akhale owerengeka.
7 Za Yuda ndi izi; ndipo anati,Imvani, Yehova, mau a Yuda,Ndipo mumfikitse kwa anthu ace;Manja ace amfikire;Ndipo mukhale inu thandizo lace pa iwo akumuukira.
8 Ndipo za Levi anati,Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu,Amene mudamuyesa m'Masa,Amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;
9 Amene anati za atate wace ndi amai wace, Sindinamuone;Sanazindikira abale ace,Sanadziwa ana ace omwe;Popeza anasamalira mau anu, Nasunga cipangano canu.
10 Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu,Ndi Israyeli cilamulo canu;Adzaika cofukiza pamaso panu,Ndi nsembe yopsereza yamphumphu pa guwa la nsembe lanu.
11 Dalitsani, Yehova, mphamvu yace,Nimulandire nchito ya manja ace;Akantheni m'cuuno iwo akumuukira,Ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.
12 Za Benjamini anati,Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi iye mokhazikika;Amphimba tsiku lonse,Inde akhalitsa pakati pa mapewa ace.
13 Ndipo za Yosefe anati,Yehova adalitse dziko lace;Ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame,Ndi madzi okhala pansipo;
14 Ndi zipatso zofunikatu za dzuwa,Ndi zomera zofunikatu za mwezi,
15 Ndi zinthu zoposa za mapiri akale,Ndi zinthu zofunikatu za zitunda zosatha,
16 Ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwace,Ndi cibvomerezo ca iye anakhala m'citsambayo;Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wace wa iye wokhala padera ndi abale ace.
17 Woyamba kubadwa wa ng'ombe yace, ulemerero ndi wace;Nyanga zace ndizo nyanga zanjati;Adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi.Iwo ndiwo zikwi khumi za Efraimu,Iwo ndiwo zikwi za Manase.
18 Ndi za Zebuloni anati,Kondwera, Zebuloni, ndi kuturukakwako;Ndi Isakara, m'mahema mwako.
19 Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri;Apo adzaphera nsembe za cilungamo;Popeza adzayamwa zocuruka za m'nyanja,Ndi cuma cobisika mumcenga.
20 Ndi za Gadi anati,Wodala iye amene akuza Gadi;Akhala ngati mkango waukazi,Namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe.
21 Ndipo anadzisankhira gawo loyamba,Popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira;Ndipo anadza ndi mafumu a anthu,Anacita cilungamo ca Yehova,Ndi maweruzo ace ndi Israyeli.
22 Ndi za Dani anati,Dani ndiye mwana wa mkango,Wakutumpha moturuka m'Basana.
23 Za Nafitali anati,Nafitali, wokhuta nazo zomkondweretsa,Wodzala ndi mdalitso wa Yehova;Landira kumadzulo ndi kumwela.
24 Ndi za Aseri anati,Aseri adalitsidwe mwa anawo;Akhale wobvomerezeka mwa abale ace,Abviike phazi lace m'mafuta.
25 Nsapato zako zikhale za citsulo ndi mkuwa;Ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.
26 Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe,Wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza,Ndi pa mitambo m'ukulu wace.
27 Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako;Ndi pansipo pali manja osatha.Ndipo aingitsa mdani pamaso pako,Nati, Ononga.
28 Ndipo Israyeli akhala mokhazikika pa yekha;Kasupe wa Yakobo;Akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo;Inde thambo lace likukha mame.
29 Wodala iwe, Israyeli;Akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova,Ndiye cikopa ca thandizo lako,Iye amene akhala lupanga la ukulu wako!Ndi adani ako adzakugonjera; Ndipo udzaponda pa misanje yao.