Deuteronomo 23 BL92

Oletsedwa ku msonkhano wa Yehova

1 Munthu wophwetekwa, wophwanyika kapena wofulika, asalowe m'msonkhano wa Yehova.

2 Mwana wa m'cigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wace wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova.

3 M-amoni kapena Mmoabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;

4 popeza sanakukumikani ndi mkate ndi madzi m'njira muja munaturuka m'Aigupto; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesapotamiya, kuti akutemberereni.

5 Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafuna kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.

6 Musawafunira mtendere, kapena cowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.

7 Musamanyansidwa naye M-edomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye M-aigupto, popeza munali alendo m'dziko lace.

8 Ana obadwa nao a mbadwo wacitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.

9 Nkhondo yanu ikaturuka pa adani anu, mudzisunge kusacita coipa ciri conse.

10 Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera cifukwa cocitika usiku, azituruka kunja kwa cigono, asalowe pakati pa cigono;

11 koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa cigono.

12 Mukhale nao malo kunja kwa cigono kumene muzimukako kuthengo;

13 nimukhale naco cokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe naco, ndi kutembenuka ndi kufotsera cakuturukaco;

14 popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa cigono canu, kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; cifukwa cace cigono canu cikhale copatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.

Za akapolo opulumuka, za acigololo, za okongoletsa mopindulitsa

15 Musamapereka kwa mbuye wace kapolo wopulumuka kwa mbuye wace kuthawira kwa inu;

16 akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m'mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.

17 Pasakhale mkazi wacigololo pakati pa ana akazi a Israyeli, kapena wacigololo pakati pa ana amuna a Israyeli.

18 Musamabwera nayo mphotho ya wacigololo, kapena mtengo wace wa garu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, cifukwa ca cowinda ciri conse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

19 Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndarama, phindu la cakudya, phindu la kanthu kali konse kokongoletsa.

20 Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m'dziko limene mulowamo kulilandira.

21 Mukawindira Yehova Mulungu wanu cowinda, musamacedwa kucicita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ici ndithu ndipo mukadacimwako.

22 Koma mukapanda kulonieza cowinda, mulibe kucimwa.

23 Coturuka pa milomo yanu mucisamalire ndi kucicita; monga munaloniezera Yehova Mulungu wanu, copereka caufulu munacilonjeza pakamwa panu.

24 Mukalowa m'munda wamphesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni koma musaika kanthu m'cotengera canu.

25 Mukalowa m'tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi zenga tirigu waciriri wa mnansi wanu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34