1 Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwacita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanu lanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu pa dziko lapansi.
2 Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri atali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;
3 nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao licoke m'malomo.
4 Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.
5 Koma ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mapfuko anu onse kuikapo dzina lace, ndiko ku cokhalamo cace, muzifunako, ndi kufikako;
6 ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;
7 ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m'mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.
8 Musamadzacita monga mwa zonse tizicita kuno lero, yense kucita ciri conse ciyenera m'maso mwace;
9 pakuti mpaka lero simunafikira mpumulo ndi colowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.
10 Koma mudzaoloka Yordano, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.
11 Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.
12 Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu.
13 Dzicenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona:
14 koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mapfuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzicita zonse ndikuuzani.
15 Koma monga mwa cikhumbu conse ca moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.
16 Mwazi wao wokha musamadya; muziuthira panthaka ngati madzi.
17 Simukhoza kudya m'mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyambakubadwa a ng'ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu ziri zonse muzilonieza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m'dzanja lanu;
18 koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.
19 Dzicenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m'dziko mwanu.
20 Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.
21 Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lace akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.
22 Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko cimodzimodzi.
23 Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yace.
24 Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi.
25 Musamadya uwu; kuti cikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu, pakucita inu zoyenera pamaso pa Yehova.
26 Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasanka;
27 ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yace muidye.
28 Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti cikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu nthawi zonse, pocita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
29 Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m'dziko lao,
30 dzicenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? ndicite momwemo inenso.
31 Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti ziri zonse zinyansira Yehova, zimene azida iye, iwowa anazicitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.
32 Ciri conse ndikuuzani, mucisamalire kucicita; musamaoniezako, kapena kucepsako.