Deuteronomo 17 BL92

1 Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala naco cirema, kapena ciri conse coipa; pakuti cinyansira Yehova Mulungu wanu.

2 Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakucita ciri coipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira cipangano cace,

3 nakatumikira milungu yina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;

4 ndipo akakuuzani, nimudamva, pamenepo muzifunsitsa, ndipo taonani, cikakhala coonadi, coti nzenizeni, conyansaci cacitika m'Israyeli;

5 pamenepo muturutse mwamunayo kapena mkaziyo, anacita coipaco, kumka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe.

6 Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi.

7 Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse, Potero muzicotsa coipaco pakati panu.

8 Ukakulakani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo mirandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kumka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;

9 nimufike kwa ansembe, Alevi, ndi kwa woweruza wa m'masiku awo; nimufunsire; ndipo adzakufotokozerani maweruzidwe ace.

10 Ndipo mucite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kucita monga mwa zonse akulangizanizi,

11 Monga momwe anena malamulo akulangizani, ndi monga mwa ciweruzo akufotokozerani, mucite; mau akufotokozerani musawapatukire kulamanja kapena kulamanzere.

12 Koma munthu wakucita modzikuza, osamvera wansembe wokhala ciriri kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo mucotse coipaco kwa Israyeli.

13 Ndipo anthu onse adzamva ndi kucita mantha, osacitanso modzikuza.

Za kusankha mfumu ndi zomuyenera

14 Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanu lanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga;

15 mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha; wina pakati pa abale anu mumuike mfumu yanu; simuyenera kudziikira mlendo, wosakhala mbale wanu.

16 Koma asadzicurukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu amke ku Aigupto, kuti acurukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.

17 Ndipo asadzicurukitsire akazi, kuti ungapatuke mtinta wace; kapena asadzicurukitsire kwambiri siliva ndi golidi.

18 Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wacifumu wa ufumu wace, adzilemberere cofanana ca cilamuloici m'buku, acitenge pa ici ciri pamaso pa ansembe Alevi;

19 ndipo azikhala naco, nawerengemo masiku onse a moyo wace; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wace, kusunga mau ons acilamulo ici ndi malemba awa, kuwacita;

20 kuti mtima wace usadzikuze pa abaleace, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti acuruke masiku ace, m'ufumu wace, iye ndi ana ace pakati pa Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34