1 Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene mumkako kulilandira likhale lanu lanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigazi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikuru ndi yamphamvu yoposa inu;
2 nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwacitira cifundo.
3 Ndipo musakwatitsane nao; musampatsemwana wace wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wace wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.
4 Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu yina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.
5 Koma muzicita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.
6 Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.
7 Yehova sanakondwera nanu, ndi kukusankhani cifukwa ca kucuruka kwanu koposa mitundu yonse yina ya anthu, kapena kucepera kwanu;
8 koma Yehova anakuturutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya akapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, cifukwa Yehova akukondani, ndi cifukwa ca kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.
9 Cifukwa cace dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga cipangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace, kufikira mibadwo zikwi.
10 Ndipo awabwezera onse akudana ndi iye, pamaso pao, kuwaononga; sacedwa naye wakudana ndi iye, ambwezera pamaso pace.
11 Potero muzisunga malamulo, ndi malemba, ndi maweruzo, amene ndikuuzani lero kuwacita.
12 Ndipo kudzakhala, cifukwa ca kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwacita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani cipangano ndi cifundo cimene analumbirira makolo anu;
13 ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukucurukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi ana a nkhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.
14 Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.
15 Ndipo Yehova adzakucotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa ziri zonse za Aigupto muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.
16 Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawacitire cifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakucitirani msampha.
17 Mukadzanena m'mtima mwanu, Amitundu awa andicurukira; ndikhoza bwanji kuwapitikitsa?
18 musamawaopa; mukumbukile bwino cimene Yehova Mulungu wanu anacitira Farao, ndi Aigupto wonse;
19 mayesero akuru maso anu anawapenya, ndi zizindikilo ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakuturutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.
20 Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mabvu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu.
21 Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkuru ndi woopsa.
22 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang'ono pang'ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakucurukireni zirombo.
23 Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapitikitsa ndi kupitikitsa kwakukuru, kufikira ataonongeka.
24 Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga,
25 Mafano osema a milungu yao muwateothe ndi moto; musamasirira siliva ndi golidi ziri pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.
26 Musamalowa naco conyansaci m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi naco; muziipidwa naco konse, ndi kunyansidwa naco konse; popeza ndi cinthu coyenera kuonongeka konse.