Deuteronomo 1 BL92

Mose awafotokozera za ulendo wao m'cipululu

1 AWA ndi mau amene Mose ananena kwa Israyeli wonse, tsidya la Yordano m'cipululu, m'cidikha ca pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofeli, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Di Zahabi.

2 Ulendo wace wocokera ku Horebe wofikira ku Kadesi Barinea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.

3 Ndipo kunali, caka ca makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israyeli, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;

4 atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, wakukhala m'Asitaroti, ku Edrei.

5 Tsidya lija la Yordano, m'dziko la Moabu, Mose anayamba kufotokozera cilamulo ici, ndi kuti.

6 Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife m'Horebe, ndi kuti, Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno;

7 bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kucidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwela, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebano, kufikira nyanja yaikuru Firate.

8 Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.

9 Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;

10 Yehova Mulungu wanu anakucurukitsani, ndipo taonani, lero mucuruka ngati nyenyezi za kumwamba.

11 Yehova Mulungu wa makolo anu, acurukitsire ciwerengero canu calero ndi cikwi cimodzi, nakudalitseni monga iye ananena nanu!

12 Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu?

13 Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akuru anu.

14 Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwacita.

15 Potero ndinatenga akuru a mapfuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akuru anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mapfuko anu.

16 Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wace, ndi mlendo wokhala naye.

17 Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akuru muwamvere m'modzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza ciweruzo nca Mulungu; ndipo mlandu ukakulakani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.

18 Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzicita.

19 Pamenepo tinayenda ulendo kucokera ku Horebe, ndi kubzyola m'cipululu cacikuru ndi coopsa ciija conse munacionaci, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi Barinea.

20 Ndipo ndinati kwa inu, Mwafikira mapiri a Aamori, amene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

21 Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamacita mantha, musamatenga nkhawa.

22 Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komweko, ndi za midzi yoti tidzafikako.

23 Ndipo cinandikomera cinthu ici; ndipo ndinatenga amuna khumi ndi awiri ainu, pfuko limodzi mwamuna mmodzi;

24 amenewa anatembenuka nakwera kumapiri nalowa ku cigwa ca Esikolo, nacizonda.

25 Ndipo anatengako zipatso za dzikoli m'manja mwao, natsikira nazo kwa ife, natibwezera mau ndi kuti, Dzikoli Yehova Mulungu wathu atipatsa ndi labwino.

26 Koma simunafuna kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu.

27 Ndipo munadandaula m'mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, iye anatiturutsa m'dziko la Aigupto, kutipereka m'manja mwa Aamori, ationonge.

28 Tikwere kuti? abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo akulu ndi atali akuposa ife; midzi ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.

29 Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamacita mantha nao.

30 Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakucitirani m'Aigupto pamaso panu;

31 ndi kucipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wace wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno.

32 Koma m'cinthu ici simunakhulupirira Yehova Mulungu wanu,

33 amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi mota usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.

34 Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,

35 Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.

36 Koma Kalebi mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ace; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.

37 Yehova anakwiya ndi inenso cifukwa ca inu, ndi kuti, lwenso sudzalowamo.

38 Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israyeli.

39 Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa cabwino kapena coipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.

40 Koma inu, bwererani, mukani ulendo wanu kucipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

41 Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tacimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira mkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zace za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kumka kumapiri.

42 Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindiri pakati panu; angakukantheni adani anu.

43 Pamene ndinanena ndi inu simunamvera; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kucita modzikuza, nimunakwera kumka kumapiri.

44 Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anaturuka kukomana ndi inu, nakupitikitsani, monga zimacita njuci, nakukanthani m'Seiri, kufikira ku Horima.

45 Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvera mau anu, kapena kukucherani khutu.

46 Potero munakhala m'Kadesi masiku ambiri, monga mwa masiku munakhalako.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34