1 Ndipo akuru a makolo a mabanja a ana a Gileadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akuru a makolo a ana a Israyeli;
2 nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israyeli dzikoli mocita maere likhale colowa cao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ace akazi colowa ca Tselofekadi mbale wathu.
3 Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mapfuko ena a ana a Israyeli, acicotse colowa cao ku colowa ca makolo athu, nacionjeze ku colowa ca pfuko limene adzakhalako; cotero acicotse ku maere a colowa cathu.
4 Ndipo pofika caka coliza ca ana a Israyeli adzaphatikiza colowa cao ku colowa ca pfuko limene akhalako; cotero adzacotsa colowa cao ku colowa ca pfuko la makolo athu.
5 Ndipo Mose analamulira ana a Israyeli monga mwa mau a Yehova, nati, Pfuko la ana a Yosefe linena zaona.
6 Colamulira Yehova za ana akazi a Tselofekadi ndi ici, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ace; komatu akwatibwe nao a banja la pfuko la makolo ao okha okha.
7 Motero colowa ca ana a Israyeli sicidzamka m'pfuko m'pfuko; popeza ana a Israyeli adzamamatira yense ku colowa ca pfuko la makolo ace.
8 Ndipo mwana wamkazi yense wa mapfuko a ana a Israyeli, wakukhala naco colowa, akwatibwe ndi wina wa banja la pfuko la kholo lace, kuti ana a Israyeli akhale naco yense colowa ca makolo ace.
9 Motero colowa ca ana a Israyeli sicidzamka m'pfuko m'pfuko, pakuti mapfuko a ana a Israyeli adzamamatira lonse ku colowa cace cace.
10 Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana akazi a Tselofekadi anacita;
11 popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana akazi a Tselofekadi, anakwatibwa ndi ana amuna a abale a atate wao.
12 Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo colowa cao dnakhala m'pfuko la banja la atate wao.
13 Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israyeli ndi dzanja la Mose m'zidikha za Moabu pa Yordano ku Yeriko.