1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,
2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mukakalowa m'dziko lokakhalamo inu, limene ndirikupatsa inu,
3 ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pocita cowinda ca padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumcitira Yehova pfungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;
4 pamenepo iye wobwera naco copereka cace kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la bini la mafuta;
5 ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la bini, ukhale wa mwana wa nkhosa mmodzi.
6 Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la bini.
7 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo atatu la bini, acitire Yehova pfungo lokoma.
8 Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kucita cowinda ca padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;
9 abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la bini.
10 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya pfungo: lokoma, ya Yehova.
11 Kudzatero ndi ng'ombe iri yonse, kapena nkhosa yamphongo iri yonse, kapena mwana wa nkhosa ali yense, kapena mwana wa mbuzi ali yense.
12 Monga mwa kuwerenga kwace kwa izi muzikonza, muzitero ndi yonse monga mwa kuwerenga kwace.
13 Onse akubadwa m'dzikomo acite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya pfungo lokoma.
14 Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena ali yense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakacitira Yehova nsembe yamoto ya pfungo lokoma; monga mucita inu, momwemo iyenso,
15 Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.
16 Pakhale cilamulo cimodzi ndi ciweruzo cimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu.
17 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
18 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Pamene mulowa m'dziko limene ndirikukulowetsani,
19 kudzali, pakudya inu mkate wa m'dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza.
20 Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumacitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza.
21 Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.
22 Ndipo pamene mulakwa, osacita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;
23 ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova anauza, ndi kunkabe m'mibadwo yanu;
24 pamenepo kudzali, ngati anacicita osati dala, osacidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya pfungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira, monga mwa ciweruzo cace; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo.
25 Ndipo wansembe azicita cotetezera khamu lonse la ana a Israyeli, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanacita dala, ndipo anadza naco copereka cao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yaucimo pamaso pa Yehova, cifukwa ca kulakwa osati dala.
26 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli, adzakhululukidwa, ndi mlendo yemwe wakukhala pakati pao; popeza khamu lonse linacicita osati dala.
27 Ndipo akacimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yamsoti ya caka cimodzi, ikhale nsembe yaucimo.
28 Ndipo wansembe acite comtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumcita comtetezeraj ndipo adzakhululukidwa.
29 Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale naco cilamulo cimodzi kwa iye wakucita kanthu kosati dala.
30 Koma munthu wakucita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo acitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wace.
31 Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lace; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yace ikhale pa iye.
32 Ndipo pokhala ana a Israyeli m'cipululu, anapeza munthu wakufuna nkhuni tsiku la Sabata.
33 Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.
34 Ndipo anathanga wamsunga, popeza sicinanenedwa coyenera kumcitira iye.
35 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa cigono.
36 Pamenepo khamu lonse linamturutsa kunja kwa cigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.
37 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
38 Nena ndi ana a Israyeli, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zobvala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi.
39 Ndipo cikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukila malamulo onse a Yehova, ndi kuwacita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi cigololo;
40 kuti mukumbukile ndi kucita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu.
41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakukuturutsani m'dziko la Aigupto, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.