Numeri 7 BL92

Zopereka za Akuru 12 atautsa cihemaco

1 Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa kacisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;

2 akalonga a Israyeli, akuru a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mapfuko akuyang'anira owerengedwa;

3 anadza naco copereka cao pamaso pa Yehova, magareta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi ng'ombe khumi ndi ziwfri; akalonga awiri anapereka gareta mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa kacisi.

4 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

5 Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakucitira nchito ya cihema cokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa nchito yace.

6 Ndipo Mose analandira magareta ndi ng'ombe, nazipereka kwa Alevi.

7 Anapatsa ana a Gerisoni magareta awiri ndi ng'ombe zinai, monga mwa nchito yao;

8 napatsa ana a Merari magareta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa nchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.

9 Koma sanapatsa ana a Kohati kanthu; popeza nchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.

10 Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka ciperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera naco copereka cao pa guwa la nsembelo.

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lace, apereke zopereka zao za kupereka ciperekere guwa la nsembe.

12 Wakubwera naco copereka cace tsiku loyamba ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu, wa pfuko la Yuda:

13 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembeyaufa;

14 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

15 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

16 ronde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

17 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa: asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Nahesoni mwana wa Aminadabu.

18 Tsiku laciwiri Netaneli mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera naco cace:

19 anabwera naco copereka cace mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

20 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

21 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

22 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

23 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Netaneli mwana wa Zuwara.

24 Tsiku lacitatu kalonga wa ana a Zebuloni, ndiye Eliyabu mwana wa Heloni:

25 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

26 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

27 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

28 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

29 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Eliyabu mwana wa Heloni.

30 Tsiku lacinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni:

31 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

32 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

33 ng'ombe yamphongo Imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

34 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

35 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Elizuri mwana wa Sedeuri.

36 Tsiku lacisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiyeli, mwana wa Zurisadai:

37 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

38 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

39 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

40 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

41 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Selumiyeli mwana wa Zurisadai.

42 Tsiku lacisanu ndi cimodzi, kalonga wa ana a Gadi, Eliyasafe mwana wa Deyueli:

43 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu; mbale yowazira Imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

44 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

45 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

46 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

47 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Eliyasafe mwana wa Deyueli.

48 Tsiku lacisanu ndi ciwiri kalonga wa ana a Efraimu Elisama mwana wa Amihudi:

49 copereka cace mbizi Imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

50 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

51 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

52 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

53 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa za mphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Elisama mwana wa Amihudi.

54 Tsiku lacisanu ndi citatu kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri:

55 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

56 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

57 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

58 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

59 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

60 Tsiku lacisanu ndi cinai kalonga wa ana a Benjamini, ndiye Abidana mwana wa Gideoni:

61 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

62 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

63 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

64 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

65 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Abidana mwana wa Gideoni.

66 Tsiku lakhumi kalonga wa ana a Dani, ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai:

67 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;

68 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

69 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

70 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

71 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

72 Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Aseri, ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani;

73 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

74 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

75 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

76 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

77 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Pagiyeli mwana wa Okirani.

78 Tsiku lakhumi ndi ciwiri kalonga wa ana a Nafitali, ndiye Ahira mwana wa Enani:

79 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

80 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

81 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

82 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

83 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ici ndi copereka ca Ahira mwana wa Enani.

84 Uku ndi kupereka ciperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israyeli, tsiku la kudzoza kwace: mbizi zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolidi khumi ndi ziwiri;

85 mbizi yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.

86 Zipande zagolidi ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi cofukiza, cipande conse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golidi wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;

87 ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, ana a nkhosa a caka cimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zaucimo khumi ndi awiri;

88 ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, ana a nkhosa a caka cimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka ciperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.

89 Ndipo polowa Mose ku cihema cokomanako, kunena ndi iye, anamva Mau akunena naye ocokera ku cotetezerapo ciri pa likasa la mboni, ocokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo iye ananena naye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36