Numeri 19 BL92

Za ng'ombe yamsoti yofiira ndi madzi oyeretsa nao

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Ili ndi lemba la cilamulo Yehova adalamuliraci, ndi kuti, Nena ndi ana a Israyeli kuti azikutengera ng'ombe ramsoti yofiira, yangwiro yopanda enema, yosamanga m'goli;

3 ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naiturutse iye kunja kwa cigono, ndipo wina aiphe pamaso pace.

4 Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wace ndi cala cace, nawazeko mwazi wace kasanu ndi kawiri pakhomo pa cihema cokomanako.

5 Pamenepo atenthe ng'ombe yamsotiyo pamaso pace; atenthe cikopa cace ndi nyama yace, ndi mwazi wace, pamodzi ndi cipwidza cace.

6 Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa mota irikupsererapo ng'ombe yamsoti.

7 Pamenepo wansembe atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi; ndipo atatero alowenso kucigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

8 Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

9 Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe ya msotiyo, nawaike kunja kwa cigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a lsrayeli akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yaucimo.

10 Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe ya msoti atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israyeli, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.

11 Iye wakukhudza mtembo wa munthu ali yense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;

12 iyeyo adziyeretse nao tsiku lacitatu, ndi pa tsiku lacisanu ndi ciwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lacitatu, sadzakhala woyera tsiku lacisanu ndi ciwiri.

13 Ali yense wakukhudza mtembo wa munthu ali yense wakufa, osadziyeretsa, aipsa kacisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israyeli; popeza sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwace kukali pa iye.

14 Cilamulo ndi ici: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

15 Ndi zotengera zonse zobvundukuka, zopanda cibvundikilo comangikapo, ziri zodetsedwa.

16 Ndipo ali yense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena pfupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

17 Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yaucimo, nathirepo m'cotengera madzi oyenda;

18 ndi munthu woyera atenge hisope, nambviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza pfupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena Manda.

19 Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lacitatu, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri; ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri amyeretse; ndipo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo.

20 Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.

21 Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zobvala zace; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

22 Ndipo ciri conse munthu wodetsedwa acikhudza cidzakhala codetsedwa; ndi munthu wakucikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36