Numeri 21 BL92

Aisrayeli aononga Akanani

1 Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwela, anamva kuti Israyeli anadzera njira ya azondi, anathira nkhondo pa Israyeli, nagwira ena akhale ansinga.

2 Ndipo Israyeli analonjeza cowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m'dzanja langa, ndidzaononga midzi yao konse.

3 Ndipo Yehova anamvera mau a Israyeli, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi midzi yao yomwe; nacha dzina lace la malowo Horima.

Njoka yamkuwa

4 Ndipo anayenda ulendo kucokera ku phiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada cifukwa ca njirayo.

5 Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kuticotsa ku Aigupto kuti tifere m'cipululu? pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wacabe uwu.

6 Pamenepo Yehova anatumiza njoka zamoto pakati pa anthu, ndipo zinaluma anthu; nafapo anthu ambiri a Israyeli.

7 Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tacimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti aticotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.

8 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Upange njoka yamoto; nulike pa mtengowace; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo.

9 Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu ali yense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.

Acoka kumka ulendo wao

10 Pamenepo ana a Israyeli anayenda ulendo, namanga mahema m'Oboti.

11 Ndipo anacoka ku Oboti, namanga mahema ku Iyebarimu, m'cipululu cakuno ca Moabu, koturukira dzuwa.

12 Pocokapo anayenda ulendo, namanga mahema m'cigwa ca Zaredi.

13 Atacokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya tina la Arinoni, wokhala m'cipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Moabu, pakati pa Moabu ndi Aamori.

14 Cifukwa cace, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova,Vahebi m'Sufa,Ndi miyendo ya Arinoni;

15 Ndi zigwa za miyendoyoZakutsikira kwao kwa Ari,Ndi kuyandikizana ndi malire a Moabu.

16 Ndipo atacokapo anamuka ku Been, ndico citsime cimene Yehova anacinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.

17 Pamenepo Israyeli anayimba nyimbo iyi:Tumphuka citsime iwe; mucithirire mang'ombe;

18 Citsime adakumba mafumu,Adacikonza omveka a anthu;Atanena mlamuli, ndi ndodo zao.Ndipo atacoka kucipululu anamuka ku Matana;

19 atacoka ku Matana ku Nahaliyeli; atacoka ku Nahaliyeli ku Bamoti;

20 atacoka ku Bamoti ku cigwa ciri m'dziko la Moabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndicipululu.

Aisrayeli alanda dziko la Aamori

21 Ndipo Israyeli anatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ndi kuti,

22 Ndipitire pakati pa dziko lako; sitidzapatuka kulowa m'munda, kapena m'munda wampesa, sitidzamwako madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wacifumu, kufikira tapitirira malire ako.

23 Ndipo Sihoni sanalola Israyeli apitire m'malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, nadzakomana naye Israyeli m'cipululu, nafika ku Jahazi, nathira nkhondo pa Israyeli.

24 Ndipo Israyeli anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lace likhale lao lao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana ai Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.

25 Ndipo Israyeli analanda midzi iyi yonse; nakhala Israyeli m'midzi yonse ya Aamori; m'Hesiboni ndi miraga yace yonse.

26 Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Moabu, nilanda dziko lace m'dzanja lace kufikira Arinoni.

27 Cifukwa cace iwo akunena mophiphiritsa akuti,Idzani ku Hesiboni,Mudzi wa Sihoni umangike, nukhazikike:

28 Popeza moto unaturuka m'Hesiboni,Cirangali ca mota m'mudzi wa Sihoni;Catha Ari wa Moabu,Eni misanje ya Arinoni.

29 Tsoka kwa iwe, Moabu!Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu,Anapereka ana ace amuna opulumuka,Ndi ana ace akazi akhale ansinga,Kwa Sihoni mfumu ya Aamori.

30 Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni,Ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa,Ndiwo wakufikira ku Medeba.

31 Comweco Israyeli anakhala m'dziko la Aamori.

32 Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda miraga yace, napitikitsa Aamori a komweko.

Aisrayeli alanda dziko la Basana

33 Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basanu; ndipo Ogi mfumu ya ku Basana anaturuka kukumana nao, iye ndi anthu ace onse, kudzacita nao nkhondo ku Edreyi.

34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ace onse, ndi dziko lace; umcitire monga umo unacitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni.

35 Ndipo anamkantha iye, ndi ana ace amuna ndi anthu ace onse, kufikira sanatsala ndi mmodzi yense; nalanda dziko lace likhale lao lao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36