Numeri 4 BL92

Akohati

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Werengani ana a Kohati pakati pa ana a Levi, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,

3 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire nchito ya cihema cokomanako.

4 Nchito ya ana a Kohati m'cihema cokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulikitsa:

5 akati amuke a m'cigono, Aroni ndi ana ace amuna azilowa, natsitse nsaru yocinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,

6 ndi kuikapo cophimba ca zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsaru yamadzi yeni yeni, ndi kupisako mphiko zace.

7 Ndi pa gome la mkate waonekera ayale nsaru yamadzi, naikepo mbale zace, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa cikhalire uzikhalaponso.

8 Ndipo ayale pa izi nsaru yofiira, ndi kuliphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.

9 Ndipo atenge nsaru yamadzi, ndi kuphimba coikapo nyali younikira, ndi nyali zace, ndi mbano zace, ndi zaolera zace, ndi zotengera zace zonse za mafuta zogwira nazo nchito yace.

10 Ndipo acimange ndi cipangizo zace zonse m'cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa conyamulira.

11 Ndipo pa guwa la nsembe lagolidi aziyala nsaru yamadzi, naliphimbe ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.

12 Natenge zipangizo zace zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsaru yamadzi, ndi kuziphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika paconyamulira.

13 Ndipo azicotsa mapulusa pa guwa la nsembe, ndi kuyala pa ilo nsaru yofiirira.

14 Naikepo zipangizo zace zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zaolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.

15 Atatha Aroni ndi ana ace amuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zace zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'cigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'cihema cokomanako.

16 Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa kacisi wonse, ndi zonse ziri m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zace.

17 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Dati,

18 Musamasadza pfuko la mabanja a Kohati kuwacotsa pakati pa Alevi;

19 koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulikitsazo; Aroni ndi ana ace amuna alowe, namuikire munthu yense nchito yace ndi katundu wace.

20 Koma asalowe kukaona zopatulikazo pozikulunga, kuti angafe.

Agerisoni

21 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

22 Werenganso ana a Gerisoni, monga mwa nyumba za makolo ao, monga mwa mabanja ao.

23 Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kucita nchitoyi m'cihema cokomanako.

24 Nchito ya mabanja a Agerisoni, pogwira nchito ndi kusenza katundu ndi iyi;

25 azinyamula nsaru zophimba za kacisi, ndi cihema cokomanako, cophimba cace, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu ciri pamwamba pace, ndi nsaru yotsekera pa khomo la cihema cokomanako;

26 ndi nsaru zocingira za pabwalo, ndi nsaru yotsekera ku cipata ca pabwalo liri pakacisi ndi pa guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za Debito zao, ndi zonse acita nazo; m'menemo muli nchito zao.

27 Nchito yonse ya ana a Agerisoni, kunena za akatundu ao ndi nchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ace amuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.

28 Iyi ndi nchito ya mabanja a ana a Gerisoni m'cihema cokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao.

Amerari

29 Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao.

30 Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kucita nchito ya cihema cokomanako.

31 Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako ndi ici: matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace;

32 ndi nsici za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ace, ndi ziciri zace, ndi zingwe zace, pamodzi ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito yace yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwaehula maina ao.

33 Iyi ndi nchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.

34 Ndipo Mose ndi Aroni ndi akalonga a khamu anawerenga ana a Akohati monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,

35 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire Debito m'cihema cokomanako;

36 ndipo owerengedwa ao monga mwa mabanja ao ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.

37 Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'cihema cokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

38 Ndipo ana owerengedwa a Gerisoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyu mba za makolo ao,

39 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire nchito m'cihema cokomanako,

40 owerengedwa ao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.

41 Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Gerisoni, onse akutumikira m'cihema cokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova.

42 Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,

43 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu kuti agwire nchito m'cihema cokomanako,

44 owerengedwa ao monga mwa mabanja ao, ndiwo zikwi zitatu ndi mazana awiri.

45 Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

Kuwerengedwa kwa Alevi

46 Owerengedwa onse a Alevi, amene Mose ndi Aroni ndi akalonga a Israyeli anawawerengera, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,

47 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira nchito ya utumikiwu, ndiyo nchito ya akatundu m'cihema cokomanako;

48 owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu mphambu makumi asanu ndi atatu.

49 Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36