Numeri 11 BL92

Kudandaula kwa Aisrayeli

1 Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi mota wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku cilekezero ca cigono.

2 Pamenepo anthu anapfuulira kwa Mose; ndi Mose anapemphera kwa Yehova, ndi motowo unazimika.

3 Ndipo anacha malowo dzina lace Tabera; popeza moto wa Yehova udayaka pakati pao.

4 Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa naco cilakolako; ndi ana a Israyeli omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?

5 Tikumbukira nsomba tinazidya m'Aigupto cabe, mankaka, ndi mavwendi, ndi anyesi a mitundu itatu;

6 koma tsopano moyo wathu waphwa; tiribe kanthu pamaso pathu koma mana awa.

7 Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ace ngati maonekedwe a bedola.

8 Anthu amamka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.

9 Ndipo pakugwa mame pacigono usiku, mana anagwapo.

Mose adandaulapa katundu wace

10 Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wace; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.

11 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munacitiranji coipa mtumiki wanu? ndalekeranii kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse?

12 Kodi ndinaima nao anthu awa onse? kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kumka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?

13 Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye.

14 Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine.

15 Ndipo ngati mundicitira cotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang'ane tsoka langa.

16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akuru a Israyeli, amene uwadziwa kuti ndiwo akuru a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku cihema cokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.

17 Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uti pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.

18 Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? popeza tinakhala bwino m'Aigupto, Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya.

19 Simudzadya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku khumi, kapena masiku makumi awiri;

20 koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pace, ndi kuti, Tinaturukiranji m'Aigupto?

21 Ndipo Mose anati, Anthu amene ndiri pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.

22 Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira?

23 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? tsopano udzapenya ngati mau anga adzakucitikira kapena iai.

24 Ndipo Mose anaturuka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akuru a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa cihema.

25 Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena nave, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akuru makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.

26 Koma amuna awiri anatsalira m'cigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzace ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanaturuka kumka kucihema; ndipo ananenera m'cigono.

27 Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'cigono.

28 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wace, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.

29 Koma Mose anati kwa iye, Kodi ucita nsanje nao cifukwa ca ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri! mwenzi Yehova atawaikira mzimu wace!

30 Ndipo Mose ndi akulu onse a Israyeli anasonkhana kucigono.

31 Ndipo kudacokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zocokera kunyanja, nizitula kucigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa cigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.

32 Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wace wonse, ndi mawa lace lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa cigono.

33 Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukuru ndithu.

34 Ndipo anacha malowo dzina lace Kibiroti Hatava; popeza pamenepo anaika anthu osusuka.

35 Kucokera ku Kibiroti Hatava anthuwo anayenda kumka ku Hazeroti; nakhala ku Hazeroti.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36