Numeri 8 BL92

Za kuyatsa nyalizo

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali manu ndi ziwirizo ziwale pandunji pace pa coikapo nyalico.

3 Ndipo Aroni anacita cotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pace pa coikapo nyali, monga Yehova adauza Mose.

4 Ndipo mapangidwe ace a coikapo nyali ndiwo golidi wosula; kuyambira tsinde lace kufikira maluwa ace anacisula; monga mwa maonekedwe ace Yehova anaonetsa Mose, momwemo anacipanga coikapo nyali.

Za kuyeretsa Alevi

5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

6 Uwatenge Alevi pakati pa ana a Israyeli, nuwayeretse.

7 Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akucotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zobvala zao, nadziyeretse.

8 Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yace yaufa, ufa wosanganiza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo yina ikhale nsembe yaucimo.

9 Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa cihema cokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israyeli;

10 nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israyeli aike manja ao pa Alevi;

11 ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yocokera kwa ana a Israyeli, kuti akhale akucita nchito ya Yehova,

12 Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yaucimo, ndi inzace, nsembe yopsereza za Yehova, kucita cotetezera Alevi.

13 Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ace, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova.

14 Momwemo upatule Alevi mwa ana a Israyeli; kuti Alevi akhale anga.

15 Ndipo atatero alowe Alevi kucita Debito ya cihema cokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula.

16 Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ocokera mwa ana a Israyeli; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula m'mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israyeli.

17 Pakuti a oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Aigupto, ndinadzipatulira iwo akhale anga.

18 Ndipo ndatenga Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli.

19 Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ace amuna yocokera mwa ana a Israyeli, kucita nchito ya ana a Israyeli, m'cihema cokomanako ndi kucita cotetezera ana a Israyeli; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israyeli, pakuyandikiza ana a Israyeli ku malo opatulika.

20 Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli anacitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a lsrayeli anawacitira.

21 Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zobvala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawacitira cotetezera kuwayeretsa.

22 Ndipo atatero, Alevi analowa kucita Debito yao m'cihema cokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ace amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawacitira.

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

24 Ici ndi ca Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu nchito ya cihema cokomanako;

25 ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osacitanso nchitoyi;

26 koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'cihema cokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira nchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36