1 Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.
2 Ndipo maina ao a ana amuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
3 Awa ndi maina a ana amuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao acite nchito ya nsembe.
4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wacilendo pamaso pa Yehova, m'cipululu ca Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anacita Debito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.
5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
6 Sendera nalo kuno pfuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.
7 Ndipo azisunga udikiro wace, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la cihema cokomanako, kucita nchito ya kacisi.
8 Ndipo asunge zipangizo zonse za cihema cokomanako, ndi udikiro wa ana a Israyeli, kuicita nchito ya kacisi.
9 Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ocokera kwa ana a Israyeli.
10 Koma uike Aroni ndi ana ace amuna, azisunga nchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
12 Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli m'malo mwa ana ovamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israyeli; ndipo Aleviwo ndi anga.
13 Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Aigupto ndinadzipatulira ana oyamba onse m'Israyeli, kuyambira munthu kufikira coweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.
14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'cipululu ca Sinai, nati,
15 Werenga ana a Levi monga mwa nyumba ya makolo ao, monga mwa mabanja ao; uwawerenge mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu.
16 Ndipo Mose anawawerenga monga mwa mau a Yehova, monga adamuuza.
17 Ndipo ana a Levi maina ao ndi awa: Gerisoni, ndi Kohati ndi Merari.
18 Ndi ana a Gerisoni maina ao ndi awa, monga mwa mabanja ao: Libini, ndi Simei.
19 Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amiramu ndi lzara, Hebroni ndi Uziyeli.
20 Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.
21 Banja la Libini, ndi mabanja a Simei, ndiwo a Gerisoni; ndiwo mabanja a Gerisoni.
22 Owerengedwa ao, powawerenga amuna onse, kuyambira mwana wa mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.
23 Mabanja a Agerisoni azimanga mahema ao pambuyo pa kacisi kumadzulo.
24 Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo a Agerisoni ndiye Eliyasafe mwana wa Layeli.
25 Ndipo udikiro wa ana a Gerisoni m'cihema cokomanako ndiwo kacisi, ndi cihema, cophimba cace, ndi nsaru yotsekera pa khomo la cihema cokomanako,
26 ndi nsaru zocinga za kubwalo, ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo, lokhala kukacisi, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zace za ku nchito zace zonse.
27 Banja la Aamiramu, ndi banja la Aizara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyeli ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.
28 Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pa malo opatulika.
29 Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumwera.
30 Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafana mwana wa Uziyeli.
31 Ndipoudikirowaondiwo likasa, ndi gome, ndi coikapo nyali, ndimagome a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene acita nazo, ndi nsaru yocinga, ndi nchito zace zonse.
32 Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pa malo opatulika.
33 Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo a Merari; ndiwo mabanja a Merari.
34 Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi kudza mazana awiri.
35 Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja a Merari ndiye Zuriyeli mwana wa Abiyaili; azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumpoto.
36 Ndipo coyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace, ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito zace zonse;
37 ndi nsici za pabwalo pozungulira, ndi makamwa ace, ndi ziciri zace, ndi zingwe zace.
38 Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la kacisi, kum'mawa, pa khomo la cihema cokomanako koturukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ace amuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israyeli; koma mlendo wakuyandikizako amuphe,
39 Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
40 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Werenga amuna oyamba kubadwa onse a ana a Israyeli kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu nuone ciwerengo ca maina ao.
41 Ndipo unditengere Ine Alevi (ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israyeli.
42 Ndipo Mose anawawerenga, monga Yehova adamuuza, oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli.
43 Ndipo amuna onse oyamba kubadwa, powerenga maina, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri mphambu atatu.
44 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
45 Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.
46 Kunena za mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza atatuwo oyamba kubadwa a ana a Israyeli, akuposa Alevi, akaomboledwe,
47 ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);
48 nupereke ndarama zimene akuposawo anaomboledwa nazo kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna.
49 Pamenepo Mose analandira ndarama zaom bola nazo kwa iwo akuposa aja adawaombola Alevi;
50 analandira ndaramazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israyeli; masekeli cikwi cimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.
51 Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ace ndarama zaom bola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.