Numeri 2 BL92

Malongosoledwe a cigono

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Ana a Israyeli azimanga mahema ao yense ku mbendera yace, ya cizindikilo ca nyumba ya kholo lace; amange mahema ao popenyana ndi cihema cokomanako pozungulira.

3 Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa koturuka dzuwa ndiwo a mbendera ya cigono ca Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Yuda ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu.

4 Ndipo khamu lace, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi.

5 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netandi mwana wa Zuwara.

6 Ndipo khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.

7 Ndi pfuko la Zebuloni: kalonga wa ana a Zebuloni ndiye Eliyabu mwana wa Heloni.

8 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.

9 Owerengedwa onse a cigono ca Yuda ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi cimodzi mphambu mazana anai, monga mwa makamu ao, Ndiwo azitsogolera ulendo.

10 Mbendera ya cigono ca Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.

11 Ndi khamu lace, ndi olembedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.

12 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiyeli mwana wa Surisadai.

13 Ndi khamu lace ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.

14 Ndi pfuko la Gadi; kalonga wa ana a Gadi ndiye Eliyasafe mwana wa Reueli.

15 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.

16 Owerengedwa onse a cigono ca Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi cimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.

17 Pamenepo khamu la Alevi azimuka naco cihema cokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pace, monga mwa mbendera zao.

18 Mbendera ya cigono ca Efraimu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efraimu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.

19 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu.

20 Ndipo oyandikizana naye ndiwo a pfuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

21 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.

22 Ndi pfuko la Benjamini: kalonga wa ana a Benjamini ndiye Abidana mwana wa Gideoni.

23 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.

24 Owerengedwa onse a cigono ca Efraimu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lacitatu paulendo.

25 Mbendera ya cigono ca Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

26 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

27 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Aseri; ndi kalonga wa ana a Aseri ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani.

28 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu cimodzi kudza mazana asanu.

29 Ndi pfuko la Nafitali: ndi kalonga wa ana a Nafitali ndiye Ahira mwana wa Enani.

30 Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

31 Owerengedwa onse a cigono ca Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi Hmodzi. Iwo ndiwo aziyenda m'mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao.

32 Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.

33 Koma sanawerenga Alevi mwa ana a Israyeli; monga Yehova adauza Mose.

34 Ndipo ana a Israyeli anacita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ace, monga mwa nyumba za makolo ace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36