1 Maulendo a ana a Israyeli amene anaturuka m'dziko la Aigupto monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.
2 Ndipo Mose analembera maturukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa maturukidwe ao.
3 Ndipo anacokera ku Ramese mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi woyamba; atacita Paskha m'mawa mwace ana a Israyeli, anaturuka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aaigupto onse,
4 pamene Aaigupto ailalikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.
5 Ndipo ana a Israyeli macokera ku Ramese, nayenda namanga ku Sukoti.
6 Nacokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a cipululu.
7 Ndipo anacokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwace kwa Baala Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.
8 Ndipo anacokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'cipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'cipululu ca Etamu, namanga m'Mara.
9 Ndipo anacokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko.
10 Ndipo anacokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira.
11 Nacokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'cipululu ca Sini.
12 Nacokera ku cipululu ca Sini, nayenda namanga m'Dofika.
13 Nacokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi.
14 Nacokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.
15 Ndipo anacokera ku Refidimu, nayenda namanga m'cipululu ca Sinai.
16 Nacokera ku cipululu ca Sinai, nayenda namanga m'Kibiroti Hatava.
17 Nacokera ku Kibiroti Hatava, nayenda namanga m'Hazeroti.
18 Nacokera ku Hazeroti, nayenda namanga m'Ritima.
19 Nacokera ku Ritima, nayenda namanga m'Rimoni Perezi.
20 Nacokera ku Rimoni Perezi, nayenda namanga m'Libina.
21 Nacokera ku Libina, nayenda namanga m'Risa.
22 Nacokera ku Risa, nayenda namanga m'Kehelata.
23 Nacokera ku Kehelata, nayenda namanga m'phiri la Saferi.
24 Nacokera ku phiri la Saferi, nayenda namanga n'Harada.
25 Nacokera ku Harada, nayenda namanga m'Makeloti.
26 Nacokera ku Makeloti, nayenda namanga m'Tahata.
27 Nacokera ku Tahata, nayenda namanga m'Tara.
28 Nacokera ku Tara, nayenda namanga m'Mitika.
29 Nacokera ku Mitika, nayenda namanga m'Hasimona.
30 Nacokera ku Hasimona, nayenda namanga m'Moseroto.
31 Nacokera ku Moseroto, nayenda namanga m'Bene Yaakana.
32 Nacokera ku Bene Yaakana, nayenda namanga m'Hori Hagidigadi.
33 Nacokera ku Hori Hagidigadi, nayenda namanga m'Yotibata.
34 Nacokera ku Yotibata, nayenda namanga m'Abirona.
35 Nacokera ku Abirona, nayenda namanga m'Ezioni Geberi.
36 Nacokera ku Ezioni Geberi, nayenda namanga m'cipululu ca Zini (ndiko Kadesi).
37 Nacokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.
38 Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto zaka makumi anai, mwezi wacisanu, tsiku loyamba la mwezi.
39 Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori.
40 Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwela m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israyeli.
41 Ndipo anacokera ku phiri la Hori, nayenda namanga m'Tsalimona.
42 Nacokera ku Tsalimona, nayenda namanga m'Punoni.
43 Nacokera ku Punoni, nayenda namanga m'Oboti.
44 Nacokera ku Oboti, nayenda namanga m'iye Abarimu, m'malire a Moabu.
45 Nacokera ku lyimu, nayenda namanga m'Diboni Gadi.
46 Nacokera ku Diboni Gadi, nayenda namanga m'Alimoni Diblataimu.
47 Nacokera ku Alimoni Diblataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, cakuno ca Nebo.
48 Nacokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m'zidikhaza Moabu pa Yordano ku Yeriko,
49 Ndipo anamanga pa Yordano, kuyambira ku Beti Yesimoti kufikira ku Abeli Sitimu m'zidikha za Moabu.
50 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Moabu pa YordaBaku Yeriko, nati,
51 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutaoloka Yordano kulowa m'dziko la Kanani,
52 mupitikitse onse okhala m'dzikopamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;
53 ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanu lanu.
54 Ndipo mulandire dzikoli ndi kucita maere monga mwa mabanja anu; colowa cao cicurukire ocurukawo, colowa cao cicepere ocepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwace; mulandire colowa canu monga mwa mapfuko a makolo anu.
55 Koma mukapanda kupitikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakubvutani m'dziko limene mukhalamo.
56 Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kucitira iwowa, ndidzakucitirani inu.