1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'cipululu ca Sinai, mwezi woyamba wa caka caciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto, ndi kuti,
2 Ana a Israyeli acite Paskha pa nyengo yoikidwa.
3 Tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, muziucita, pa nyengo yace yoikidwa; muucite monga mwa malemba ace onse, ndi maweruzo ace onse.
4 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, kuti acite Paskha.
5 Ndipo anacita Paskha mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, m'cipululu ca Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israyeli anacita.
6 Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoza kucita Paskha tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;
7 nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, pakati pa ana a Israyeli?
8 Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve couza Yehova za inu.
9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10 Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, cifukwa ca mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azicitira Yehova Paskha.
11 Mwezi waciwiri, tsiku lace lakhumi ndi cinai, madzulo, aucite; audye ndi mkate wopanda cotupitsa ndi msuzi wowawa.
12 Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo pfupa; aucite monga mwa lemba lonse la Paskha.
13 Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kucita Paskha, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wace; popeza sanabwera naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, munthuyu asenze kucimwa kwace.
14 Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakacitira Yehova Paskha, azicita monga mwa lemba la Paskha, ndi monga mwa ciweruzo cace; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.
15 Ndipo tsiku loutsa kacisi mtambo unaphimba kacisi, ndiwo cihema cokomanako; ndipo madzulo padaoneka pakacisi ngati moto, kufikira m'mawa.
16 Kudatero kosalekeza; mtambo umaciphimba, ndimoto umaoneka usiku,
17 Ndipo pokwera mtambo kucokera kucihema, utatero ana a Israyeli amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israyeli amamanga mahema ao.
18 Pakuwauza Yehova ana a Israyeli amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa kacisi amakhala m'cigono.
19 Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa kacisi, pamenepo ana a Israyeli anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.
20 Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa kacisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'cigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.
21 Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo; ngakhale msana ngakhale usiku, pokwera mtambo, ayenda ulendo.
22 Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa kacisi ndi kukhalapo, ana a Israyeli anakhala m'cigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
23 Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose.