1 Ndipo Miriamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose cifukwa ca mkazi mtundu wace Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.
2 Ndipo anati, Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? sananenanso ndi ife nanga? Ndipo Yehova anamva.
3 Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriamu modzidzimutsa, Turukani inu atatu kudza ku cihema cokomanako. Pamenepo anaturuka atatuwo.
5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la cihema, naitana Aroni ndi Miriamu; naturuka onse awiri.
6 Ndipo anati, Tamvani tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.
7 Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.
8 Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, maonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.
9 Pamenepo Mulungu anawapsera mtima iwo; nawacokera iye.
10 Ndipo mtambo unacoka pacihema; ndipo taonani, Miriamu anali wakhate, wa mbu ngati cipale cofewa; ndipo Aroni anapenya Miriamu, taonani, anali wakhate.
11 Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kucimwa kumene tapusa nako, ndi kucimwa nako.
12 Asakhaletu iye ngati wakufa, amene dera lina la mnofu wace watha poturuka iye m'mimba mwa mace.
13 Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mciritsenitu, Mulungu,
14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wace akadamlabvulira malobvu pankhope pace sakadacita manyazi masiku asanu ndi awiri? ambindikiritse kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.
15 Pamenepo anambindikiritsa Miriamu kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayenda ulendo kufikira atamlandiranso Miriamu.
16 Ndipo atatero anthuwo anamka ulendo wao kucokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'cipululu ca Parana.